MALONGOSOLEDWE AMAYIMBIDWE By Chisomo Dan Kauma



Comments



Description

Vol.I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 NKHOMA SYNOD Church of Central Africa Presbyterian LILONGWE PRESBYTERY MUSIC COMMITTEE VOL. I Golden Rules for Congregation Conductors CONDUCTING TECHNIQUE CCAP (FEB, 2018) PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. DAN Kauma PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma Vol. I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 MALAMULO OFUNIKA KUTSATILA POFUNA KUKWEZA MAYIMBIDWE MUMPINGO 1. CHOLINGA CHACHIKULU CHA MAYIMBIDWE MUMPINGO Cholinga chachikulu chakuyimba mu Mpingo ndicho kulemekeza Mulungu, ndikumuyamika Iye. Poonjeza apo, kuyimba kumathandiza kutakasa mtima kuti anthu adzipeleke kwa Mulungu mwakusiya zoipa zimene zimawasiyanitsa ndi Mulungu. 2. UBWINO WAKUYIMBA MUMPINGO 2.1. Oyimba amalumikizika ndi Mulungu m’kuyimba, chifukwa amazama m’maganizo ndikumvetsetsa za Mulungu kusiyana ndi pamene palibe kuyimba. 2.2. Oyimba amatulutsa zakukhosi kwawo kudzera mkuthamanga kwake kwa nyimbo, kukweza kwake, liwu lake, kulumikizika kwa mawu, komanso manvekedwe ake a nyimbo. 2.3. Kuyimba kumakongoletsa chipembedzo. Mumpingo, nyimbo zake zimapatsa aliyense mwayi wakutula kwa Mulungu liwu lake la pamtima, lomwe angakhale nalo. Ichi chimachitika ndi iye amene ali m’chipembedzo. 3. MAYIMBIDWE Mayimbidwe ake a nyimbo ndi osiyanasiyana malingana ndi nyengo yake kapenanso cholinga chake. Chitsanzo, pa nthawi ya ukwati mayimbidwe ake amakhala osiyana ndiponso nkhope za oyimbawo zidzasiyana monga mwa nyengo yake. Maliwu anyimbo ayenera kugwirizana ndinyengo zake. Maliwu apamaliro kapena pa ukwati kapena pa chipembedzo aziwonetsa kusiyana pakukweza kwake. Mwa chitsanzo, pamene tikumbukira za imfa ya Ambuye wathu Yesu Khristu. Maliwu ofanana ndi amaliro angathe kuyimbidwa. 4. WOTSOGOLERA NYIMBO PA CHIPEMBEDZO 4.4. Amawongolera onse kuti mayimbidwe amveke bwino. Ndikuti nyimbo izithamanga moyenera monga mwachikhalidwe cha nyimbo yomwe ikayimbidwa. Wotsogolera nyimbo ndi amene amapeleka maganizo (mood) anyimbo kuti ikhudze kapena kusintha womvera ndiponso woyimba. 4.5. Amathandiza kuti anthu asamangokokerana kapena kulimbirana poyambitsa nyimbo. Kapena potsogolera mizère ina m’ndime za nyimbo. Muchizungu (Solo, Duet, Trio, Quartet ndi Choir). 4.6. Wotsogolerayo akhale wambiri yabwino. Asakhale munthu yemwe amamveka mbiri zoyipa ku mpingo kapena kudera kumene amakhala, kapena kumene amagwira ntchito ya muofesi kapena ya malonda. Chifukwa izi zimatsekereza kapena kuchotsa chidwi kwa anthu omvera ndi woyimbitsidwa zimene zikaletsa kupititsa patsogole uthenga wabwino. PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma Vol. I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 4.7. Akhale wodziwa bwino maliwu anyimbo ndikutsogolera kwake. Kapena kuti akhale odziwa nyimbo zambiri komanso amene amatha kuwerenga nyimbo muziyankhulo izi: Choyamba, Staff Notation kapena kuti zibonga, chachiwiri ndichomaliza ndi Tonic Sol-fah kapena kuti “do do do”. Chitsanzo onani pansi: Figure 1. Music Scale/Ladder 4.8. Akhale wa mawu omveka bwino kapena kuti anthetemnya. Chifukwa chake ndichakuti, anthu oyimba kawirikawiri amatengera mtsogoleri mmene achitira. Ngati mtsogoleri ayimba mokadzula, mpingonso udzatengera zomwezo powona ngati ndiko kuyimba koyenera 4.9. Akhale wodziwa bwino momwe nyimbo iyenera kufulumirira osati wogoneka nyimbo kapenanso wokhadzulira poyimba ayi. 4.10. Akhale pamalo oti wonse adzimuwona. 4.11. Adzivala bwino osati mochititsa manyazi. Ngati mkutheka, avale Jaketi komanso abophe mabatani monga chitsanzo chili m’musimu. Figure 2. Mavalidwe Achimuna 4.12. Azikhala ndi tcheru pakuyimbitsa kuti awonetsetse kuti anthu akuyimba mogwirizana bwino osati mokweza munthu payekha. (Balancing mu chizungu) 4.13. Ayenera kuimirira bwino pamalo owonekera 4.14. Akonzekere “Key” ya nyimbo imene yatchulidwa (Zina nyimbo ndi zokwera, zina ndi zotsika komanso zina ndi zachikatikati). Chitsanzo cha ma “Key” anyimbo zonse zapadziko lapansi PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma Vol. I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 Figure 3. Ma "Key" anyimbo 4.15. Liwiro la nyimbo (Speed) ndi kufulumira, kuchedwa ndi pakatikati (fast, slow, ndi moderate). Izi ndi mwazina mugulu la liwiro la nyimbo (Speed). Zitsanzo zina onani pansi: Figure 4. Mwa mawu ena a Liwiro la nyimbo m’mchizungu 4.16. Aphunzitse anthu kuti aziwona mabiti (Beat/Conducting) 4.17. Wotsogolera aziphunzitsa nyimbo zimene siziyimbidwayimbidwa 5. MALONGOSOLEDWE APATSIKU LA MULUNGU 5.5. Woyimbitsa nyimbo pa Sabata ali ndi magawo awa: 5.5.1. Wolalikira akalonjera msonkhano, woyimbitsa nyimbo ndiye ayambe nyimbo yoti: Yesu Mbuye Onani, Tadza poitana inu 5.5.2. Wotsogolera asayambitse ndiye “Pemphero la Ambuye”Limeneli ndigawo la wolalikira kuyambitsa 5.5.3. Nyimbo yolemekeza iyambidwe ndi Woyambitsa nyimbo 5.5.4. Wolalikira akatha kuwerenga Malamulo khumi kapena Chiphatikizo cha malamulo khumi, ndikunena za kulapa ndi chikhululukiro, Woyimbitsa nyimbo ndiye atsogolere nyimbo yonena zakulapa. PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma Vol. I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 5.5.5. Chikhulupiliro cha chikhrisitu amene amayambitsa ndi Wolalikira osati Woyimbitsa nyimbo ayi. 5.5.6. Woyimbitsa nyimbo ndiye amayambitsa nyimbo mpingo utatha kunena Chikhulupiliro cha Chikhristu CHENJEZO: Woyambitsa nyimbo asalowerere nthawi ya wolalikira ayi, uku ndikupewa chisokonezo 1. Mayambidwe ndi matsilizidwe a nyimbo akhale bwino ndipo pomaliza nyimboyo onse atsilizire pamodzi 2. Wotsogolera nyimbo asayambe nyimbo anthu asanadziwe kapena asanapeze nyimboyo ayi 3. Nyimbo zoyimba pa chipembedzo zilembedwe ndikuikidwa pamalo owoneka kuti onse azikonzekeratu. Nyimbo ziyambe zaphunzitsidwa chipembedzo chisanayambe 4. Wolalikira azilengeza nambala ya nyimbo momveka bwino kuti onse amve ndikupezeratu 5. Wolalikirayo awerenge ndime yoyamba ndi kolasi kupereka mpata woti anthu apeze nyimbo 6. Ngati yemwe alalikira ali ndi liwu lina la nyimboyo lomwe iye afuna kuti mpingo uyimbe, amuuziletu wotsogolera nyimbo nthawi ya chipembedzo isanakwane kuwopa 6. MABITI (BEATS/CONDUCTING) A NYIMBO ZIMENE TIMAYIMBA Wotsogolera nyimbo azidziwa kuti nyimbo zili ndi mabiti ake. Afunika kutsatira mabitiwo kuti nyimbo ziziyenda bwino. Zitsanzo za mabitiwa ndi izi: 1. Mabiti awiri 3. Mabiti atatu 4. Mabiti anayi 2. (2 Beats): 2/4 (3 Beats): 3/4 (4 Beats): 4/4 PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma Vol. I Malangizo Ofunika Kutsatira Pofuna Kukweza Mayimbidwe FEB 2018 Mabitiwa amapitilira apa (Onani zitsanzo tsamba lomaliza), zimayenera munthu woyimbitsa nyimbo kuchita kafukufuku nthawi zonse. Chitsanzo, pakakhala maphunzilo mumpingo kapena kwina, azitengapo mbali kuti aziwonjezera luso. Woyimbitsa nyimbo asamavina poyimbitsa nyimbo koma asamalire za mabiti a nyimbo kuti mpingo uyende pamodzi m’mayimbidwewo. 7. ZOWONJEZEREKA (APPENDIX) 1. Kuchita Chitsanzo (Conducting Patterns) PREPARED BY (Okonza): Mr. D.E. Lubayini & Mr. C. Dan Kauma
Copyright © 2024 DOKUMEN.SITE Inc.